2 Kings 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake mfumu Yowasi adaitana wansembe Yehoyada ndi ansembe ena, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza Nyumbayi? Kuyambira tsopano, musasungenso ndalama za anthu amene mumaŵatumikira, koma muzipereke kuti akonzere Nyumbayi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu Yoasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndarama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.