2 Kings 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, mwana wa Ahaziya mfumu ya ku Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu, adayamba kulamulira Aisraele ku Samariya, ndipo adakhala mfumu zaka 17.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi awiri ndi zitatu cha Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu analowa ufumu wake wa Israele ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Yoasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yoahazimwana wa Yehu analowa ufumu wace wa Israyeli ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.