2 Kings 13:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene adazichita, kudzanso zamphamvu zimene adaonetsa pomenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono a Yowasi, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake yochita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono a Yoasi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yocita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?