2 Kings 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo Elisa adadwala matenda ofa nawo, ndipo Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamzonda. Adakalira misozi pamaso pake nkumati, “Atate, atate! Magaleta a Israele ndiponso okwerapo ake!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yowasi mfumu ya Israele, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, galeta wa Israele ndi apakavalo ake!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yoasi mfumu ya Israyeli, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace!