2 Kings 13:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Elisa adauza Yehowasi mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Kokani utawu.” Iye nkukokadi. Apo Elisayo adaika manja ake pa manja a mfumuyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa mfumu ya Israele, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ake pa manja a mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa mfumu ya Israyeli, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ace pa manja a mfumu.