2 Kings 13:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo adati, “Tsekulani windo lakuvuma.” Ndipo adatsekuladi. Tsono Elisa adati, “Ponyani.” Yehowasi nkuponya. Pomwepo Elisa adati, “Inuyo ndinu muvi wa Chauta wogonjetsera pa nkhondo, muvi wogonjetsera Asiriya. Pakuti mudzamenyana nawo nkhondo Asiriya ku Afeki mpaka kuŵatha onse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Muvi wa chipulumutso wa Yehova ndiwo muvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Mubvi wa cipulumutso wa Yehova ndiwo mubvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.