2 Kings 13:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adati, “Tengani mivi inayo.” Yehowasi adaitenga. Tsono Elisa adauza mfumu ya ku Israele ija kuti, “Lasani pansi miviyo.” Ndipo iye adalasa pansi katatu, nkuleka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Tengani mivi; naitenga. Nati kwa mfumu ya Israele, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.