2 Kings 13:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Aisraele ena kuti akaike mnzao ku manda, adangoona gulu lankhondo la Amowabuwo, iwo nkungoponya mtembowo m'manda mwa Elisa. Munthu wakufayo atangokhudza mafupa a Elisa, pomwepo adatsitsimuka nakhala chilili.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima chilili.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.