2 Kings 13:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta adaŵakomera mtima Aisraelewo ndi kuŵamveranso chifundo. Adaŵalezera mtima chifukwa cha chipangano chimene Iye adaachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, choncho sadalole kuti adani aŵaononge. Ndipo sadaiŵale anthu akewo mpaka tsopano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova analeza nao mtima, nawachitira chifundo, nawatembenukira; chifukwa cha chipangano chake ndi Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova analeza nao mtima, nawacitira cifundo, nawatembenukira; cifukwa ca cipangano cace ndi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pace.