2 Kings 13:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, adalandanso kwa Benihadadi, mwana wa Hazaele, mizinda imene Benihadadiyo anali atailanda pomenyana nkhondo ndi Yehowahazi bambo wa Yehowasi. Yehowasi adagonjetsa Benihadadi katatu, nalandanso mizinda yonse ya Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi Yehowasi mwana wa Yehowahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wake ndi nkhondo. Yowasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi Yoasi mwana wa Yoahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wace ndi nkhondo. Yoasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israyeli.