2 Kings 13:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta adakwiyira Aisraele, ndipo kaŵirikaŵiri adalola kuti Hazaele mfumu ya ku Siriya ndiponso Benihadadi mwana wa Hazaeleyo aŵagonjetse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israele, nawapereka m'dzanja la Hazaele mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaele, masiku onsewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israyeli, nawapereka m'dzanja la Hazaeli mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli, masiku onsewoo