2 Kings 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehowahazi adapemphera kwa Chauta ndipo Chauta adamumvera, poti adaona kupsinjidwa kwa Aisraele kumene mfumu ya ku Siriya idaŵapsinja nako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehowahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwake kwa Israele m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwace kwa Israyeli m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.