2 Kings 13:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Yehowahazi analibe gulu lankhondo lalikulu. Anali ndi asilikali a pa akavalo makumi asanu okha, magaleta khumi ndiponso asilikali oyenda pansi zikwi khumi, popeza kuti mfumu ya ku Siriya inali itaononga asilikali ambiri nkuŵaponderezeratu ngati fumbi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu ya Aramu sanasiyire Yehowahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magaleta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati fumbi lopondapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu ya Aramu sanasiyira Yoahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magareta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati pfumbi lopondapo.