2 Kings 14:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Amaziya sadasamaleko zimenezi. Motero Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda ku Betesemesi m'dziko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Amaziya sanamvere zimenezi. Choncho Yehowasi mfumu ya Israeli anakamuthira nkhondo. Yehowasi ndi Amaziya anakumana maso ndi maso ku Beti-Semesi mʼdziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Amaziya sanamvera. Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.