2 Kings 14:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Yehowasi adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mafumu a ku Israele ku Samariya. Ndiye Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Yerobowamu mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehowasi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo mwana wake Yeroboamu analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagona Yoasi ndi makolo ace, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Yerobiamu mwana wace.