2 Kings 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti anthu ena adaapangana zomchita chiwembu Amaziyayo ku Yerusalemu, iye nkuthaŵira ku Lakisi. Adani akewo adatuma anthu omlondola, nakamphera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anapangana zomuchita chiwembu mu Yerusalemu ndipo Amaziya anathawira ku Lakisi, koma anatumiza anthu ku Lakisiko nakamuphera komweko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.