2 Kings 14:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo anthu onse a ku Yuda adatenga Azariya, mwana wake, namlonga ufumu m'malo mwa Amaziya bambo wake. Azariyayo anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya, amene anali ndi zaka 16 namulonga ufumu mʼmalo mwa abambo ake Amaziya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya,