2 Kings 14:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azariya adagonjetsa mzinda wa Elati naumanganso nkuubwezera ku dziko la Yuda, bambo wake atamwalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Azariya anamanga mzinda wa Elati ndi kuwubwezeretsa ku Yuda, Amaziya atamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, atagona ndi makolo ace mfumuyo.