2 Kings 14:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 15 cha ufumu wa Amaziya, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adaloŵa ufumu ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 42.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha khumi ndi chisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yeroboamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israeli analowa ufumu ku Samariya ndipo analamulira za 41.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka cakhumi ndi zisanu ca Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda, Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli analowa ufumu wace m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu cimodzi.