2 Kings 14:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalandanso madera ena amene kale anali a dziko la Israele, kuyambira ku chipata cha Hamati kumpoto mpaka kumwera kukafika ku Nyanja ya Araba. Motero zidachitikadi zimene Chauta, Mulungu wa Israele, adaalankhula kudzera mwa Yona mtumiki wake, mwana wa Amitai, mneneri wa ku Gatihefere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ndi amene anabwezeretsanso malire a Israeli kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, molingana ndi zimene ananena Yehova Mulungu wa Israeli, kudzera mwa mtumiki wake Yona mwana wa Amitai, mneneri wochokera ku Gati-Heferi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anabweza malire a Israyeli kuyambira polowera ku Hamati mpaka nyanja ya kucidikha, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wace Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gati-heferi,