2 Kings 14:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta sadaanena kuti adzafafaniza ufumu wa Israele pa dziko lapansi ai. Motero adaŵapulumutsa Aisraele kudzera mwa Yerobowamu mwana wa Yehowasi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yowasi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova anali asananene zofafaniza ufumu wa Israeli pa dziko lapansi, Iye anawapulumutsa kudzera mʼdzanja la Yeroboamu mwana wa Yowasi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israyeli pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobiamu mwana wa Yoasi.