2 Kings 14:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Amaziya adachita zolungama pamaso pa Chauta, komabe osati nthaŵi zonse monga Davide kholo lake. Ankachita zonse monga m'mene ankachitira Yowasi bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi zomwe anachita Davide kholo lake. Iye anatsatira zochita zonse za Yowasi abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lace; nacita monga mwa zonse anazicita Yoasi atate wace.