2 Kings 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
potsata zimene zidalembedwa m'malamulo a m'buku la Mose, m'mene Chauta adalamula kuti, “Atate sadzaphedwa chifukwa cha ana ao, kapena ana kuphedwa chifukwa cha atate ao. Koma aliyense adzafera machimo ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu iye sanaphe ana a anthu amene anapha abambo ake potsatira zomwe zinalembedwa mʼbuku la Malamulo a Mose. Mʼmenemo Yehova analamula kuti, “Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ana a ambandawo sanawapha, monga mwalembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulak wa kwa iye yekha.