2 Kings 14:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehowasi, mfumu ya ku Israele, adabweza mau kwa Amaziya, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Padangotere, mtungwi wa ku Lebanoni udaatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amkwatire.’ Koma chilombo cha ku Lebanoni chidadzera pomwepo, nkuupondereza mtungwiwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehowasi mfumu ya Israeli anabweza mawu kwa Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Mtengo wa minga wa ku Lebanoni unatumiza uthenga kwa mkungudza wa ku Lebanoni. ‘Patse mwana wako wamkazi kuti ndimukwatire.’ Kenaka chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa mingawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natumiza Yoasi mfumu ya Israyeli kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; ndipo Inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebano, nipondereza mtungwiwo.