2 Kings 15:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Izi ndi zimene Chauta adalonjeza Yehu, adati, “Ana ako aamuna adzalamulira Aisraele mpaka mbadwo wachinai.” Ndipo zidachitikadi momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndiwo mawu a Yehova amene anayankhula kwa Yehu kuti, “Ana ako adzalamulira Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.