2 Kings 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo, kuchokera ku Tiriza Menahemu adakaononga mzinda wa Tapuwa ndi anthu onse amene anali m'menemo, kuphatikiza dziko lonse lozungulira, poti iwo sadamgonjere. Adaphanso akazi apathupi amumzindamo naŵang'amba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo Menahemu, kuchokera ku Tiriza, anakathira nkhondo mzinda wa Tipisa ndi anthu onse amene anali mʼmenemo ndi dera lonse lozungulira chifukwa iwo anakana kutsekula zipata zawo. Iye anatenga katundu yense mu mzinda wa Tipisa ndi kutumbula akazi onse oyembekezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Menahemu anakantha Tifisa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ace kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulira pacipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.