2 Kings 15:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 39 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Menahemu mwana wa Gadi adaloŵa ufumu wa ku Israele, ndipo adalamulira zaka khumi ku Samariya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira mu Samariya zaka khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wace wa Israyeti, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.