2 Kings 15:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Menahemu ankachita zoipa kuchimwira Chauta. Masiku onse a moyo wake sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Nthawi yonse ya ulamuliro wake sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita coipa pamaso pa Yehova masiku ace onse, osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.