2 Kings 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Pulo, mfumu ya ku Asiriya, adadzathira nkhondo dziko la Israele. Ndipo Menahemu adakapereka kwa Pulo siliva wokwanira makilogramu 34,000, kuti Puloyo amthandize kukhazikitsa ufumu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Puli mfumu ya ku Asiriya inadzathira nkhondo dzikolo ndipo Menahemu anapatsa Puliyo makilogalamu 34,000 a siliva kuti amuthandize ndi kulimbikitsa ufumu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Puli mfumu ya Asuri anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Puli matalente a siliva cikwi cimodzi; kuti dzanja lace likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lace.