2 Kings 15:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 50 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.