2 Kings 15:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Peka mwana wa Remaliya nduna yake, pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi, adapangana za chiwembu napha Pekahiya ku Samariya m'chipinda choteteza nyumba ya mfumu. Pambuyo pake Pekayo adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Peka mwana wa Remaliya, mtsogoleri wake wa ankhondo, anamuchita chiwembu. Iye pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi anapha Pekahiya pamodzi ndi Arigobu ndi Ariyeli mʼchipinda choteteza nyumba ya mfumu mu Samariya. Kotero Peka anapha Pekahiya ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wace, anamcitira ciwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobo ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya ku nyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Gileadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwace.