2 Kings 15:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 52 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Peka mwana wa Remaliya adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka makumi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira zaka makumi awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi asanu mphambu ziwiri ca Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.