2 Kings 15:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ya Peka mfumu ya ku Israele, Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adadzagonjetsa mizinda iyi: Iyoni, Abele-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi, Hazori, dziko la Giliyadi ndi la Galilea, ndiponso dziko lonse la Nafutali. Ndipo anthu onse am'menemo adaŵagwira ukapolo, napita nawo ku Asiriya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya Peka mfumu ya Israeli, Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kudzalanda Iyoni, Abeli-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi ndi Hazori. Mfumu ya ku Asiriya inatenga Giliyadi ndi Galileya, kuphatikizanso madera onse a Nafutali ndipo anatumiza Aisraeli ku Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku a Peka mfumu ya Israyeli anadza Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, nalanda Ijoni, ndi Abeli-BeteMaaka, ndi Yanoa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Gileadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafitali; nawatenga andende kumka nao ku Asuri.