2 Kings 15:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Hoseya mwana wa Ela adachita chiwembu kuchitira mfumu Peka, namupha. Ndipo iyeyo adaloŵa ufumu m'malo mwake pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Hoseya mwana wa Ela anachitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya. Anamukantha ndi kumupha ndipo anakhala mfumu mʼmalo mwake mʼchaka makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamcitira ciwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwace caka ca makumi awiri ca Yotamu mwana wa Uziya.