2 Kings 15:38 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yotamu adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo, mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Ahazi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m'malo mwake Ahazi mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ace, namuika pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; nakhala mfumu m'malo mwace Ahazi mwana wace.