2 Kings 15:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adailanga mfumuyo ndi nthenda ya khate mpaka kufa kwake, ndipo inkakhala m'nyumba yakeyake yapadera. Choncho Yotamu mwana wa mfumuyo ndiye amene ankayang'anira banja la mfumu, namalamulira anthu m'dzikomo m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.