2 Kings 15:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 38 cha ufumu wa Azariya mfumu ya ku Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu, adaloŵa ufumu wa Aisraele ku Samariya kwa miyezi isanu ndi umodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 38 cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi isanu ndi umodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobiamu anakhala mfumu ya Israyeli m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.