2 Kings 16:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mfumu Ahazi adapita ku Damasiko kuti akakumane ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya, adaonako guwa kumeneko. Tsono adatumizira wansembe Uriya chitsanzo chake cha guwalo ndi maonekedwe ake, osasiyapo nkanthu komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe chithunzithunzi chake, ndi chifanizo chake, monga mwa mamangidwe ake onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Ahazi anamuka ku Damasiko kukakomana ndi Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, naona guwa la nsembe linali ku Damasiko; natumiza mfumu Ahazi kwa Uriya wansembe cithunzithunzi cace, ndi cifanizo cace, monga mwa mamangidwe ace onse.