2 Kings 16:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumuyo idapereka nsembe yopsereza ndi chopereka cha chakudya. Idathiranso nsembe yake yachakumwa, ndipo idawaza magazi a nsembe yake yamtendere paguwapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nafukiza nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yaufa, natsanulira nsembe yake yothira, nawaza mwazi wa nsembe zake zamtendere pa guwa la nsembelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya chakudya. Inapereka nsembe yachakumwa ndi kuwaza magazi a nsembe yake yachiyanjano paguwapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nafukiza nsembe yace yopsereza ndi nsemba yace yaufa, natsanulira nsembe yace yothira, nawaza mwazi wa nsembe zace zamtendere pa guwa la nsembelo,