2 Kings 16:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumu Ahazi adachotsa guwa lamkuŵa limene linali lomangira Chauta, pakati pa guwa lake ndi Nyumba ya Chauta, ndipo adalisuntha nakalikhazika chakumpoto kwa guwa lakelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalichotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova, nalichotsa ku khomo la nyumba pakati pa guwa la nsembe lake ndi nyumba ya Yehova, naliika kumpoto kwa guwa la nsembe lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Guwa lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo, kulichotsa pakati pa guwa latsopano ndi Nyumba ya Yehova ndi kukaliyika cha kumpoto kwa guwa latsopanolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalicotsa guwa la nsembe lamkuwa linali pamasopa Yehova, nalicotsa kukhomo la nyumba pakati pa guwa la nsembe lace ndi nyumba ya Yehova, naliikakumpotokwa guwa la nsembe lace.