2 Kings 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumuyo idalamula wansembe kuti, “Pa guwa lalikululo uperekepo nsembe zopsereza zam'maŵa, ndiponso chopereka chamadzulo cha chakudya. Uziperekanso nsembe zopsereza ndi nsembe zaufa za mfumu, ndiponso za anthu a m'dziko monsemo, pamodzi ndi zopereka za chakumwa. Ndipo pa nsembezo uwazepo magazi onse a nsembe zopsereza ndi a nsembe zonse. Koma guwa lamkuŵalo ndidzaligwiritsa ntchito poombeza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Pa guwa la nsembe lalikulu uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yake yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uriya kuti, “Pa guwa lalikulu latsopano uziperekapo nsembe yopsereza ya mmawa ndi nsembe ya chakudya ya madzulo, nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake ya chakudya ndiponso nsembe za anthu onse a mʼdziko, za chakudya ndi chakumwa. Pa guwali uziwazapo magazi a nsembe zonse zopsereza ndi nsembe zina zonse. Koma ine ndizigwiritsa ntchito guwa lansembe lamkuwa pofuna kufunsira nzeru.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Ahazi analamulira Uriya wansembe, kuti, Pa guwa la nsembe lalikuru uzifukiza nsembe yopsereza yam'mawa, ndi nsembe yaufa yamadzulo, ndi nsembe yopsereza ya mfumu, ndi nsembe yace yaufa, pamodzi ndi nsembe yopsereza ya anthu onse a m'dziko, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira; uziwaza pa ilo mwazi wonse wa nsembe yopsereza, ndi mwazi wonse wa nsembe yophera; koma guwa la nsembe lamkuwa ndi langa, lofunsira nalo.