2 Kings 16:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake mfumu Ahazi adamasula mafulemu a maphaka, nachotsapo beseni. Ndipo chimbiya chimene chinali pamwamba pa ng'ombe zamkuŵa adachitsitsa ndi kuchikhazika pa maziko amiyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nachotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa zili pansi pake, naziika pa chiunda chamiyala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Ahazi anachotsa maferemu a maphaka nachotsapo mabeseni. Iye anatsitsa mbiya yayikulu imene inali pamwamba pa ngʼombe zamkuwa ndipo anayika pansi pa chiwundo cha miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Ahazi anadula matsekerezo a maphaka, nacotsa mbiya pamwamba pao, natsitsa thawale pamwamba pa ng'ombe zamkuwa ziri pansi pace, naziika pa ciunda camiyala.