2 Kings 16:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo chifukwa chofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya, adachotsa kadenga ka pamwamba pa mpando waufumu kamene anali atakamanga m'kati mwa Nyumba ya Chauta, ndiponso adatseka khomo la panja pamene mfumu inkaloŵera m'Nyumbamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachotsa kunyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, chifukwa cha mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacotsa ku nyumba ya Yehova malo ophimbika a pa Sabata adawamanga kunyumba, ndi polowera mfumu pofuma kunja, cifukwa ca mfumu ya Asuri.