2 Kings 16:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahazi anali wa zaka 20 pamene adaloŵa ufumu ndipo adalamulira zaka 16 ku Yerusalemu. Iyeyo sadachite zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene Davide kholo lake ankachitira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; koma sanachite zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wake, ngati Davide kholo lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ahazi anali wa zaka makumi awiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; koma sanacita zoongoka pamaso pa Yehova Mulungu wace, ngati Davide kholo lace;