2 Kings 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma adatsata zitsanzo zoipa za mafumu a ku Israele. Adapereka mwana wake wamwamuna ngati nsembe yopsereza potsatira miyambo yonyansa ya anthu a mitundu ina imene Chauta adaaipirikitsa m'dzikomo pamene ankafika Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israele, napititsanso mwana wake pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza anayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, napititsanso mwana wace pamoto, monga mwa zonyansa za amitundu amene Yehova anawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli.