2 Kings 16:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Rezini mfumu ya ku Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya ku Israele adabwera kudzathira nkhondo Yerusalemu namzinga Ahazi ndi zithando zankhondo, koma sadathe kumgonjetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, anakwera kunka ku Yerusalemu kukachita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoze kumgonjetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, anakwera kumka ku Yerusalemu kukacita nkhondo, nammangira Ahazi misasa; koma sanakhoza kumgonjetsa.