2 Kings 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Rezini mfumu ya ku Edomu adapirikitsa Ayuda ku Elati, nalanda mzindawo, kuubwezera kwa Aedomu, ndipo iwo adakhala kumeneko mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napirikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komwemo kufikira lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo Rezini mfumu ya Aramu anatenganso Elati ndi kumubwezera kwa Aaramu, nathamangitsa anthu a ku Yuda mu Elatimo. Aedomu anapita kukakhala ku Elati ndipo akukhalako mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyo Rezini mfumu ya Aramu anabwezera Elati kwa Aramu, napitikitsa Ayuda ku Elati; nadza Aaramu ku Elati, nakhala komweko kufikira lero lino.