2 Kings 16:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Ahazi adatuma amithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya kukanena kuti, “Ine ndine mwana wanu ndiponso mtumiki wanu. Bwerani mudzandipulumutse kwa mfumu ya ku Siriya ndi kwa mfumu ya ku Israele, amene akundithira nkhondo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israyeli anandiukirawo.