2 Kings 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Ahazi adatenga siliva ndi golide amene adampeza m'Nyumba ya Chauta ndi mosungira chuma cha ku nyumba ya mfumu, namtumiza kwa mfumu ya ku Asiriya kuti zikhale ngati mphatso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anamupeza mʼNyumba ya Yehova ndi mosungira chuma cha nyumba ya mfumu ndi kutumiza ngati mphatso kwa mfumu ya ku Asiriya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natenga Ahazi siliva ndi golidi wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asuri.