2 Kings 17:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 12 cha ufumu wa Ahazi mfumu ya ku Yuda, Hoseya mwana wa Ela adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya. Ndipo adalamulira zaka zisanu ndi zinai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka chakhumi ndi ziwiri cha Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoseya mwana wa Ela anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka zisanu ndi zinayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka cakhumi ndi ziwiri ca Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.